Eksodo 29:39 - Buku Lopatulika39 Mwanawankhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201439 Mwanawankhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa39 Mwanawankhosa wina uzimpereka m'maŵa, wina madzulo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero39 Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Paguwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.