Eksodo 29:38 - Buku Lopatulika38 Koma izi ndizo uzikonza paguwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201438 Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa38 “Pa guwa lansembe uziperekapo izi: nthaŵi zonse tsiku ndi tsiku, uzipereka anaankhosa aŵiri a chaka chimodzi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero38 “Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri. Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.