Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 20:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Adauza Mose kuti, “Muzilankhula ndi ife ndinu, ndipo tidzamva. Mulungu asalankhule nafe, kuti tingafe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 20:19
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.


Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.


Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.


Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;


Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe.


monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu mu Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.


(ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti:


ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa