Danieli 7:19 - Buku Lopatulika19 Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake; Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 “Kenaka ndinafuna kudziwa tanthauzo lenileni la chirombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse ndi choopsa kwambiri, cha mano ake achitsulo ndi zikhadabo zamkuwa; chirombo chimene chinapweteka ndi kumeza zinazo ndi kupondaponda chilichonse chimene chinatsala. Onani mutuwo |
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.