Danieli 6:8 - Buku Lopatulika8 Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.” Onani mutuwo |
Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.
Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikize choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.