Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:38 - Buku Lopatulika

38 Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Mʼmalo mwa onsewo, idzachitira ulemu mulungu wachitetezo; mulungu wosadziwika ndi makolo ake. Iyo idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, ndi miyala yokongola, ndiponso mphatso za pamwamba kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:38
8 Mawu Ofanana  

Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.


Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena chokhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.


Ndipo adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wachilendo; aliyense womvomereza adzamchulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wake.


Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa;


Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,


malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa