Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Chivumbulutso 3:3 - Buku Lopatulika

3 Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono kumbukirani zimene mudaphunzira, ndi zimene mudamva. Muzisunge ndipo mutembenuke mtima. Mukapanda kudzuka, ndidzabwera mwadzidzidzi ngati mbala, mwakuti nthaŵi imene ndidzakupezeniyo simudzaidziŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho, kumbukira zimene unalandira ndi kumva; uzisunge ndipo ulape. Koma ngati sudzuka, ndidzabwera ngati mbala ndipo sudzadziwa nthawi imene ndidzabwere kwanu.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 3:3
24 Mawu Ofanana  

Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita.


Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu.


Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.


Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake.


kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo.


Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.


Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;


Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.


Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani;


Okondedwa, iyi ndiye kalata yachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)


Koma chimene muli nacho, gwirani kufikira ndikadza.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.


Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeze ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa