Chivumbulutso 1:2 - Buku Lopatulika2 amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Yohaneyo wafotokoza zonse zimene adaziwona, ndipo wachitira umboni mau a Mulungu, ndiponso zonse zimene Yesu Khristu adanena. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.