Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 2:5 - Buku Lopatulika

5 koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za mu Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za m'Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Yuda, ndipo motowo udzapsereza malinga a Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ine ndidzatumiza moto pa Yuda, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 2:5
11 Mawu Ofanana  

natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.


Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.


Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa mizinda yamalinga; koma ndidzatumizira mizinda yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu.


koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi.


Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake padziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha.


Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa; ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa