Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 1:16 - Buku Lopatulika

16 pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 1:16
29 Mawu Ofanana  

Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.


Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.


Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.


anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.


Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?


Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye.


Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwe kanthu kalikonse kolengedwa.


Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.


Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,


a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.


koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.


kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.


Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.


Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.


kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,


amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse;


mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za mu Mwamba.


ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro;


atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa