Ahebri 8:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye: Pakuti onse adzadziwa Ine, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye: Pakuti onse adzadziwa Ine, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake, kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti, ‘Udziŵe Ambuye’. Pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake, kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye chifukwa onse adzandidziwa, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Onani mutuwo |
Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo.