Ahebri 11:4 - Buku Lopatulika4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Pokhala ndi chikhulupiriro, Abele adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana ya Kaini, navomerezedwa kuti ngwolungama, chifukwa Mulungu mwiniwake adaamchitira umboni pakulandira zopereka zake. Mwakuti ngakhale iye adafa, koma chifukwa cha chikhulupiriro chakecho, akulankhulabe mpaka pano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho. Onani mutuwo |