2 Samueli 7:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisraele, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisraele, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Mudadzikhazikitsira anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anuanu mpaka muyaya. Ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo. Onani mutuwo |
Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?