Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 13:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 13:2
5 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye.


Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.


Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.


Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa