2 Mbiri 1:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Solomoni adalankhula ndi Aisraele onse, atsogoleri a anthu zikwi ndiponso atsogoleri a anthu mazana, aweruzi, atsogoleri a Aisraele onse, ndiponso akulu a mabanja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja. Onani mutuwo |
Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.