Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 4:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku lina mkazi wa mmodzi wa m'gulu la aneneri adapita kwa Elisa. Adampempha mokweza kuti, “Mwamuna wanga, amene anali mtumiki wanu, adamwalira. Ndipo inu mukudziŵa kuti mtumiki wanuyo ankaopa Chauta. Tsono kwafika munthu amene mwamuna wanga adakongola zinthu zake, ndipo akuti atenge ana anga aŵiri, kuti akhale akapolo ake chifukwa cha ngongoleyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 4:1
35 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.


Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;


Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.


Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.


Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.


Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete.


Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani.


Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.


Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.


ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.


Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;


Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu.


atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole;


Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.


Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.


Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.


Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.


Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.


Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, aang'ono ndi aakulu.


Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa