Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsiku lomwelo Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yeriko.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adakafika ku Yeriko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.” Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 2:4
10 Mawu Ofanana  

M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.


Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele.


Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.


Ndipo analowa, napyola pa Yeriko.


ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;


Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.


Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.


Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga;


Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa