Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mafumu 13:2 - Buku Lopatulika

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Iyeyo adachita zoipa kuchimwira Chauta. Zoipa zomwe Yerobowamu mwana wa Nebati adachimwitsa nazo Aisraele sadazileke ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 13:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.


Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.


Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.


Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo.


Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; ndipo chifanizocho chinatsalanso mu Samariya.


Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa