2 Akorinto 7:11 - Buku Lopatulika11 Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Onani zimene chisoni chanu chokomera Mulungu chija chakuchitirani: chakupatsani changu chachikulu, chakukakamizani kwambiri kutsimikiza kuti simudalakwe, chakukwiyitsani kwambiri, ndipo chakuchititsani mantha aakulu. Chakulakalakitsani kuti mundiwone, ndipo chakupatsani changu chonditchinjiriza, ndiponso cholanga olakwa. Pa nkhani yonseyi umboni ulipo wakuti inu simudalakwepo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa. Onani mutuwo |