Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Yohane 4:2 - Buku Lopatulika

2 M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: aliyense wovomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu, ameneyo ndi wochokera kwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 4:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


(ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo tichita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife);


Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso.


Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.


ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa