1 Samueli 6:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m'chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m'chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Nthaŵiyo anthu a ku Betesemesi ankadula tirigu m'chigwa. Ndipo pamene adati tha, napenya Bokosi lachipanganolo likubwera, adakondwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. Onani mutuwo |