Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 27:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndipo Akisi adamkhulupirira Davide namaganiza kuti, “Davide wadzisandutsa munthu woipa wodedwa ndi anthu ake omwe Aisraele. Nchifukwa chake adzakhala mtumiki wanga pa moyo wake wonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 27:12
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.


Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.


Ndipo Davide sadasunge wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.


Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa