Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 26:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:5
10 Mawu Ofanana  

Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.


Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Chifukwa chake Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Saulo anabwera ndithu.


Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa