Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 24:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 24:16
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.


Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.


Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo.


Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.


Mau oongoka si ndiwo amphamvu? Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani?


Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu.


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni.


Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.


Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa