Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 2:6 - Buku Lopatulika

6 Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chauta amadzetsa imfa ndipo amabwezeranso moyo, amatsitsira ku manda, ndipo amaŵatulutsakonso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo, amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 2:6
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.


Ndipo kunali atawerenga kalatayo mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine.


Pakuti apweteka, namanganso mabala; alasa, ndi manja ake omwe apoletsa.


Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni.


Imbirani Yehova, inu okondedwa ake, ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.


Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.


Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.


mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israele.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu.


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa