1 Samueli 2:33 - Buku Lopatulika33 Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha paguwa langa la nsembe, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201433 Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa33 Komabe pabanja pako ndidzasungapo mmodzi wodzanditumikira pa guwa langa, azidzangokuliritsa ndi kukumvetsa chisoni mumtima mwako. Koma ena onse a banja lako adzaphedwa ku nkhondo akali anyamata abiriŵiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero33 Komabe pa banja lako mmodzi yekha ndidzamuleka wosamuchotsa kuti azidzanditumikira. Iyeyu azidzakuliritsa ndi kukumvetsa chisoni. Koma ena onse pa banja lako adzafa akanali aangʼono.” Onani mutuwo |