Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 12:9 - Buku Lopatulika

9 Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma makolo anuwo adaiŵala Chauta, Mulungu wao. Ndipo Mulungu adaŵapereka m'manja mwa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a mzinda wa Hazori. Adaŵaperekanso m'manja mwa Afilisti ndi m'manja mwa mfumu ya ku Mowabu. Adani onsewo adachita nkhondo ndi makolo anuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 12:9
15 Mawu Ofanana  

monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.


Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao, amene anachita zazikulu mu Ejipito;


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.


Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.


Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.


Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova.


Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israele.


Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.


Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa