Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 1:2 - Buku Lopatulika

2 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Elikanayo anali wamitala, mkazi wina dzina lake anali Hana, winayo anali Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 1:2
13 Mawu Ofanana  

Koma Sarai anali wouma; analibe mwana.


Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.


Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.


Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.


Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine.


Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.


Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba.


Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,


Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.


Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa