1 Akorinto 4:9 - Buku Lopatulika9 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Ndikuwona kuti atumwife Mulungu adatipatsa malo a kuthungo kwenikweni, ngati anthu oti akukaphedwa. Ndithu tasanduka ngati chinthu chochiwonetsa kwa zolengedwa zonse, osati anthu okha ai, komanso ndi angelo omwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. Onani mutuwo |