Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:44 - Buku Lopatulika

44 lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Thupi loikidwa m'manda, ndi lamnofu chabe, koma likadzauka, lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi lamnofu, palinso thupi lauzimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:44
5 Mawu Ofanana  

Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.


Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.


Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu.


Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.


Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa