Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 1:25 - Buku Lopatulika

25 Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Chifukwa kuti chipusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 1:25
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.


Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.


Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.


Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.


Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.


pakuti anapachikidwa mu ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa