kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
Yuda 1:2 - Buku Lopatulika Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu achulukitse chifundo chake, mtendere wake ndi chikondi chake kwa inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifundo, mtendere ndi chikondi zikhale nanu mochuluka. |
kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu.
kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.
Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.