Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
Numeri 8:13 - Buku Lopatulika Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uŵauze Aleviwo kuti azitumikira Aroni ndi ana ake aamuna, ndipo uŵapereke kwa Chauta ngati chopereka choweyula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. |
Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.
Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi.
Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.