Numeri 7:48 - Buku Lopatulika Tsiku lachisanu ndi chiwiri kalonga wa ana a Efuremu Elisama mwana wa Amihudi: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lachisanu ndi chiwiri kalonga wa ana a Efuremu Elisama mwana wa Amihudi: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lachisanu ndi chiŵiri linali la Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa Aefuremu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa fuko la Efereimu, anabweretsa chopereka chake. |
Wa ana a Yosefe: wa Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri.
Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele.
chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;