Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.
Numeri 7:26 - Buku Lopatulika chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; |
Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa.
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosakaniza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;