Numeri 4:31 - Buku Lopatulika Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimene iwo alamulidwa kuti anyamule pa ntchito yao ya m'chihema chamsonkhano nazi: anyamule mitengo ya malo opatulika monga mafulemu ake, mizati yake ndi masinde ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde, |
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako.
ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.