nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.
Numeri 36:3 - Buku Lopatulika Ndipo akakwatibwa nao ana aamuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati akwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisraele, choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha makolo athu ndi kuwonjezera pa choloŵa cha fuko la amuna aowo, motero choloŵa chathu chidzachepa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa. |
nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake aakazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.
Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu.