Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito.
Numeri 33:10 - Buku Lopatulika Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adanyamuka ku Elimu, nakamanga mahema ao m'mbali mwa Nyanja Yofiira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. |
Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito.
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.