Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.
Numeri 30:16 - Buku Lopatulika Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso za bambo ndi mwana wake wamkazi amene akadali mtsikana wokhalabe m'nyumba ya bambo wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo. |