Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.
Numeri 30:14 - Buku Lopatulika Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira. |
Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.