Numeri 27:22 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adachitadi monga momwe Chauta adamlamulira. Adamtengadi Yoswa namuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anachita monga Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa ndi kumuyimiritsa pamaso pa Eliezara wansembe ndi pamaso pa gulu lonse. |
Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.