Numeri 26:37 - Buku Lopatulika Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana aamuna a Yosefe monga mwa mabanja ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneŵa, anthu okwanira 32,500, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a ana aamuna a Efuremu, zidzukulu za Yosefe potsata mabanja ao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo. |
Ana aamuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;