Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
Numeri 17:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose adatulutsa ndodo zonse zija pamaso pa Chauta ndi kuŵaonetsa Aisraele. Ataona, mtsogoleri aliyense adatenga ndodo yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, n'kutulutsa timaani, ndi kuchita maluwa, n'kubereka akatungurume.