Numeri 17:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adauza Mose kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova anawuza Mose kuti, |
Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.