Monga mwa kuwerenga kwake kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwake.
Numeri 15:13 - Buku Lopatulika Onse akubadwa m'dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onse akubadwa m'dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbadwa zonse zizichita motero pamene zikupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. |
Monga mwa kuwerenga kwake kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwake.
Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso,