Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 13:19 - Buku Lopatulika

ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri mizindayo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri midziyo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mukaone ngati dziko limene akukhalamolo ndi labwino kapena loipa, ngati mizinda imene amakhalamo ndi yamahema kapena yamalinga.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga?

Onani mutuwo



Numeri 13:19
3 Mawu Ofanana  

ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.


mukaone dziko umo liliri; ndi anthu akukhala m'mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofooka, ngati achepa kapena achuluka;


ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.