Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa chihema,
Numeri 10:11 - Buku Lopatulika Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa chihema cha mboni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa Kachisi wa mboni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa chaka chachiŵiri, mwezi wachiŵiri, tsiku la 20, mtambo udachoka pa chihema chaumboni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni. |
Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa chihema,
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa.
Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.
Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife mu Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;