Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?
Nehemiya 2:2 - Buku Lopatulika Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha aakulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha akulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo mfumu idandifunsa kuti, “Kodi bwanji nkhope yako ili yakugwa, pamene sukudwala? Chimenechi si china, koma ndi chisoni chamumtima.” Pamenepo ndidaopa kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.” Ine ndinachita mantha kwambiri. |
Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero?
Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo.