Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.
Mateyu 18:2 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayitana kamwana kakangʼono ndi kukayimiritsa pakati pawo. |
Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.
Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.
Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?
nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.