Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 13:1 - Buku Lopatulika

Ndipo pamene analikutuluka Iye mu Kachisi, mmodzi wa ophunzira ake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo pamene analikutuluka Iye m'Kachisi, mmodzi wa ophunzira ake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pamene Yesu ankachoka ku Nyumba ya Mulungu, wophunzira wake wina adamuuza kuti, “Aphunzitsi, taonani kukongola kwake miyalayi ndi nyumbazi.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”

Onani mutuwo



Marko 13:1
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse,


Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndili chipenyere, pakuchoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa chitseko cha chipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova.


Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.